BFF Malawi
Chichewa Language

Kuyenda ndi YesuKuyenda ndi Yesu

Kukhala mwa Khristu

Rev. Paul J. Bucknell

M'mene zidayambira zonse!
Iyi siidali ndondomeko yochita kukonzekera! Ambuye adandidzidzimutsa, Iwo adalowerera mchizolowezi changa ndi cholinga chofuna kundisendeza kufupi ndi iwowo.

Choyamba, Ambuye adafikira moyo wanga wodzipereka, Iwo adandikumbutsa ine chidwi changa chodziwikiratu chofuna kukula m'chikhristu. Ambuye sadakhuzike ndi utumiki wanga wofikira kutali kapena ntchito ya ubusa. Ambuye cholinga chawo chinali chopitiriza kuukonza mtima wanga. Iwo adandilankhula kudzera Masalimo 1 ndi Yoswa 1 zakufunikira kolingalira tsiku ndi tsiku.

Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako, koma ulingalire usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru (yoswa 1:8).

Mulungu analinganiza kuti kulingilira ndi njira yopangitsa anthu kukula ndi kupambana.

Moyo wodzitchinga woti ndiribe nthawi yokwanira sunapite patali. Ndinali wotanganidwa kwambiri ndi zochita zambiri komanso ndinali wokonzekera kukakumana nawo mammawa. Mulungu ankafuna nthawi yokwanira. Ndinadziwa chomwe Iye ankafuna.

Nditatha kulimbalimba, potsiriza ndinagonjera osakalankhula pa wailesi ndi cholinga choti ndimvetsere kwa Mulungu kudzera Mmau ake. Nthawi yolingirira sinayenera kukhala yochuluka tsiku liri lonse (ndidalibe nthawi yokwanira), koma ndinayenera kukhala wodzipereka mwachizolowezi. Sindinawinde, koma monga zizolowezi zina zabwino, ndinaganiza zokomana ndi Mulungu monga mmene ndingathere panthawi yina. Sindikadantha kuyerekezeratu zomwe zikanayenera kuchitika. Koma ndikaganiza za chimenechi.

Ndine wodabwabe ngakhale tsopano, patatha zaka kuchokera panthawiyo, ndine wokhudzika kwambiri pakungoganizira zomwe Mulungu anachita. Pamwamba pa zonse, ndinali kufuna kuti ndimve kuchokera kwa Ambuye panthawi ya pango’no yolingirira. Ndidazichita, Mulungu anadza pafupi nane kotero kuti ndinasinthikiratu. Sizichitikachitika kuti nthawi yipose choonadi momveka bwino, mobaya ndi kuswa mtima kufika poti ndinayenera kudzikonzekeretsa ndekha ndisanakumane naye Mulungu.

Ndinadabwa ndikuti kodi anena zotani? Kodi anditsogolera kuti? Moyo wanga sunakhalenso chimodzimozi potsatira nthawi yokhala naye kudzera mmau ake. Ndipo ponena zoona, moyo wanga sunakhaledi chimodzimodzi. Ndidadzipereka powerenga za Yesu ndi mauthenga. Mauthenga anali ozolowereka kwa ine nchocho ndinawafikira mwa njira ina Potinso, ndalalikira ndi kuphunzitsa mauthenga ambiri. Panthawi iyi, chomwe ndinkachita kunali kuwerenga mmadera mmene ndimaona Yesu akuphunzitsa ophunzira ake. Mmalo mowerenga za momwe Yesu anali kuchitira pamalo osiyanasiyana, ine ndinali kuonetsetsa zomwe ophunzirawo adaona ndi kumva. Makamaka, Yesu anali kuphunzitsa ophunzira ake.

Mauthenga adakhala ngati ulendo wathunthu wamdziko, pophunzira njira za padera. Ndimatha kukhala pa mapazi a Yesu polowa mmalo a ophunzira maso anga nd makutu kuphunzira mmene Yesu anali kuphunzitsira. Ndinafuna kuphunzitsidwa. Ichi nchomwe ndinkachikhumba. Kodi ndikadatha kuphunzira mmachitidwe oterewa? Zoonadi, ndikadatha. Ndinaphunzira zambiri, makamaka ndinene kuti, ndinali kumva kudzadzidwa ndi choonadi chomwe chanakhudza moyo wanga. Ndinaopa makamaka kuti zomwe nadikanaphunzira mmawa lake zikanaposera zomwe ndikanatha kuzikwanitsa.

Ine sindikayikanso kuti Mulungu akufuna kulankhula ndi ine kapena a Khristu ena. Iye akufuna kulankula momveka ndi mowoneka. Funso lenileni ndi loti mwina tikufuna kuti Mulungu alankhuledi kwa ife kodi ndife ofunitsitsa motani kuti Mulungu atilankhule? Nthawi yolingirira iri yonse inali yopambana ngakhale kafikidwe ka ndondomeko izi kamafanana. Matsirizidwe akukomana kwanga ndi Mulungu anali kutha ndi mphambvu yayikulu ndi kukhudza kwa moyo wanga. Nthawi zina mfundo yofunika inkatuluka nthawi yomweyo. Ziphunzitso zinali zosavuta kuzigwira. Panthawi zina, mwanjira ina Ambuye amatha kundiyesa ine. Ndinafika pophunzira pamodzimodzi kufikira atandiyankhula. Ambuye anali kukulitsa chikhulupiriro changa kotero ndinafika podziwitsitsa kuti Mulungu anali okhoza ndi okhumba kundilankhula kupyolera mzolembedwa mmau ake. Mosalabadira mamvekedwe a zolembedwa, Mulungu anali okonzekera ndi okhoza kundilankhula.

Koma ndinayenera kukangamira. Sindinayenere kutembenuza tsamba. Sindinayenera kupita ku tsamba lina. Ndinayenera kulingalira pa mau amene Mulungu adandilamulira kulingalira, ngakhale mauwo anangofikiridwa.

Pamene Mulungu adapanikiza chidwi changa pondibvumbulitsira choonadi mmau ake, mwanjira ili yonse ndinayenere kulapa. Gawo la mau liri lonse lidakhala londitsegula maso anga a uzimu pa bvuto langa la uzimu. Ndidakhala Mkhristu kwa zaka zambiri, koma ziphunzitsozi zinafikira pa mfundo yoti zinandionetsa kukhala wosunthidwa kwambiri kupyolera nkuwerenga Baibulo. Koma ndithudi zinali zoposera ku werenga Baibulo. Ine ndidakumana ndi Mulungu, kapena ndinene Mulungu adali atakumana nane mkati mwenimweni mwa zosowa za mtima wanga zomwe sindinali kuzidziwa. Makumanidwewo anali enieni zinali monga mzimu ananditengadi ndi kukandifikitsa pamalo pomwe ophunzira amapenyerera Yesu kapena kumafunsa iye mafunso. Mzimu anandipangitsa kuti ndione zomwe Yesu amazifikira. Iye kawirikawiri ndiponso mwamphabvu anali kundilankhula mu nthawi zimenezi, kotero zandipanga ine wokhulupirira wolimba ndi kufunikira kokhala Mkristu wonkhwima wokula msiknhu tsiku liri lonse mmoyo wake. Monga Paulo Mtumwi, ife sitinafikirebe pakukhala a ngwiro. Tiri ndi mwayi waukulu kwambiri kuti tikule msinkhu kuposera momwe timaganizira.

“Abale ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira: koma chinthu chimodzi ndi chichita; poyiwaladi za mmbuyo, ndikutambalitsira za mtsogolo” .Aftlipi 3:13

Nthawi yophunzira iri yonse ndinali kupenyerera pa gawo la mau. Ndinali kuwerenga ndi kulingalirapo kufikira Mulungu anali kundilankhula kudzera mmau ake. Nthawi zina izi zinali kutenga nthawi yotalikirapo kusiyana ndi nthawi zina, koma ndimakhalabe pompo mpaka mfundo ya choonadi yibvumbulukire mmoyo mwanga. Kawiri kawiri ndinali kuyesedwa kuti ndisalingalire mau ndi kungokhutitsidwa ndi kuwerenga monga mwa chizolowezi. Ndikuyamika Ambuye, ndinali kupirirabe kukakamira kuti mpaka andilankhule pa ndime ndinali kuwerengayo. Nthawi zambiri, posiyana ndi nthawi zina, ndinayenera kuwerenga popenyerera kamodzi pena kawiri choonadi cha Mulungu chimayamba yokhala pamaso pa Ambuye yimatha ndi kugwiritsa zophunzirazo pa ine. Mwachizolowezi, izi sizinali zobvuta. Iye amakhalapo kundiphunzitsa ine. Ndimati ndikalapa kuuma kwa mtima wanga, panali kukhala choonadi chomwe chimachitika ku moyo wanga.

Maphunziro ambiri amachitidwe otere alembedwa mndondomeko izi, Kuyenda ndi Yesu: Kukhala mwa Khrisyu. Chiyembekezo changa ndi choti inu muphunzira mmene mungamvere Mulungu akulankhula.

Kwa inu kudzera mmau ake. Zidzakhala nthawi zopambana zomwe mudzakhala nazo mmoyo wanu. Ambuye all kudikirira kuti alankhule kwa inu ndi ine. Watilangiza kale kuti tiziringalira mau ake. Siyani ma TV, ma Komputa ndi makanema pambali. Khalani pansi ndipo mtsimikizireni Ambuye kuti akulankhuleni kudzera mmau ake. Iye ndi okhulupirika. Mungokumbukira mafungulo. Chilichonse chomwe akuuzani kuchita, muyenera kuchita. Ndi moyo wodzipereka, koma wofunika, kuyandikira ndi mtima, kumene kumapangitsa kulingalira Baibulo kukhala nthawi yaulendo wosatha.

Zomwe Zimachitika Pokhala mwa Khristu

Tikufuna kukhala moyo wachikhristu wokwanira pomayenda ndi Yesu koma kambiri timapezeka wokhomudwitsidwa mkati mwa ulendo. Mwina chifukwa chimodzi cha chimenechi ndi choti Yesu anafotokoza modziwika, koma kutanthauzira kwa mchingerezi kuti ‘kukhala’ ‘kukhazikika’ kapena 'kukhala mwa' sizikutha kutionetsera tanthauzo lenileni la mau a Yesu.

Sipangakhale moyo, palibenso chomwe tingachimve, poyerekeza ndi chimwemwe chomwe chimadza tikakhala mwa Khristu.

Zipatso zanga za mpesa ziri ndi mitengo yayikulu komwe nthambi zazitaii zinamera. Machitidwe omwe nthambizi zidalumikizidwa (Kukhala ku thunthu la mtengo wa mpesa, ndi mmene Yesu anali kufotokozera mmene ana ake ayenera kukhala moyo wathunthu wa chikhristu. Kukhala ndichisonyezo cha kulumikizika, kulunzanitsidwa, kukhala nthambi, kugwirira ntchito limodzi, kudalira pamene zotsatira zache ndi zipatso zazikulu ndi zokongola.

Mitu

“Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zache: wakukhala mwa
Ine, ndi Ine mwa Iye, ameneyo abala chipatso chambiri;
pakuti popanda Ine simungathe kuchita kanthu” .(Yohane 15:5)

Ndinaganizira kuti zikhoza kukhala bwino kwa ife kuti tigawane zomwe takumana nazo ndi kudutsamo paulendo ndi Yesu. Ndipo ngati ulendo wosangalatsa simunauyambe, chonde uyambeni. Timayamba ndi kumudziwa Yesu. Iye anauka kwa akufa ndipo ndi wamoyo. Kukumana kumeneku ndi Iye kumatifikitsa pakuona momwe kuyipa kwa machimo athu aliri. Timamva chisoni chifukwa cha machiniowo ndipo sitimafunanso kukhala wochimwa. Ife kudzera mwa Yesu timapempha ndipo tima peza chikhululukiro. Timapitirirabe panjira ya dongosolo pokhala womvera malamulo ake. Tikakhala panjira yimeneyi timayenera kukhalabe panjirayi ndi Yesu. Timatcha "Kuyenda ndi Yesu" kapena "'Kukhala mwa Khristu." Timakhala moyo wodziwa ndi wodalira.
Pakupezeka kwa Ambuye kulikonse tingapite. Moyo umakhala wathunthu wosangalatsa. Tsiku liri lonse limakhala loyenda ndi Yesu. Ubale uliwonse, chokumana nacho ndi zochitika zimakhala zopambana.

Bwerani zazamitseni kamvedwe kanu kammene mungayendere ndi Yesu. Werengani zotsatirazi kapena makamaka yambanipo kulingalira mau a Mulungu inu nokha. Iye akuyembekezera kukumana nanu, ndi kukutengerani paulendo wodabwitsa. Ngakhale muyenera kumenya nkhondo mpaka misozi, simukanafuna kukhala wosafuna kukumana naye.

Bwerani mudzazamitse kamvedwe kanu ka mmene mungayendere ndi Yesu Yohane 15.

Kuyenda ndi Yesu: Kukhala Mwa Khristu

Chiyambi Yohane 15:5
Njira yodabwitsa yomwe Ambuye adafotokozera motsindika ndondomeko izi.

Chikondi Chosatheka Marko 8:1-9
Yesu adakwaniritsa zofunika zawo. Ophunzira anakwaniritsa zosowa zawo.

Ubwenzi weni-weni Yohane 15:15-16
Sindifuna atate wanga wa kumwamba andichite ngati mmene ndinachitira mwana wanga!

Supa ya Chikondi Marko 14:1-9
Ubale wathu ndi Mulungu ukhale wopambana kuposa ntchito yathu.

Kutsatira sichophweka Marko 10:46-52
Ndinkafuna kuti Yesu akhale ndi Ine koma sindinafunitsitsedi kuti ndikhale ndi lyeyo.

Kumvetsera mosamalitsa Marko 7:17-18
Ambuye akufuna ine ndikhale pansi ndi kumamvetsera kwa Iwo.

Chikhulupiriro cha phindu
Sindinali kutsimikizira ndi mapemphero angati anangotayika pachabe.

Kupenyetsetsa mokhazikika Mateyu 15:21-28
Yesu adadziwa kuti misonkhano yokonzekera ikhoza kusokonezeka mwa chipongwe.

Kuchitululdra chuma Marko 10:21-27
Ndi chiani chomwe iwo anadabwa ndi kuzizya nacho?

Kuyenera mzonse Marko 10:28-31
Ophunzira ake ankayembekezeka kupereka dipo la mtundu wina uli wonse mwanjira imodzi kapena zonse.

Kugadabuzika kwa chipembedzo Marko 3:1-6
Mipingo yambiri sinali kufuna kuti Yesu akhalepo!

Banja la Yesu Marko 3:31-35
Kodi inu kapena Ine tikanakhala pa gulu limeneli sitikadateronso?

Kukula Mchikhulupiriro mwa Yesu Marko 7:31-37
Ndi Yesu uti ndi kumtsatira?

Mau onena zakuzumika kwa Mkhristu Yohane 15:1-2
Sitinachite cholakwa chirichonse kuti atisadze!

Kupembedza koyenera Marko 12:28-34
Chirichonse chosamangidwa pa lamulo limodzi ili mchoperewera pa umoyo uwu.

Maloto mpaka ku mfumbi 911 Marko 13:1-3
Yesu anamva kukakamizika kutengera maloto awo ku mfumbi.

Chikhulupiriro cha ntchito Marko 11:27-33
Dziko limayamba kukhala lokhudzika pamene mpingo uyamba kuchita chikhulupiriro chake.

Kugwa kwa mbiri ya munthu Marko 2:1-2
Ndidayima mnjira zanga. Nthawi yothana ndi chikhumbo chofuna kutchuka.

Kumvetsetsa za kudandaula Luka 12:25-26
Ndife odabwa kwambiri pa ndemanga za Yesu zokhudza kudandaula.

Kugonjetsa mantha amunthu Marko 11:27-39
Kupambanidwa ndi gulu. Kuzingidwa ndi unyinji. Kuposedwa ndi maphunziro. Kunyengerera kumamphepha Yesu kuti agonjere.

 

=> The Making of a Godly Leader => Kapangidwe ka Mtsogoleri Wa Umulungu

Index to BFF's Malawi and Chichewa Videos, audio mp3s and articles


Top of page | Email us |BFF Homepage | Family Index


Biblical Foundations for Freedom