BFF Malawi

Chichewa Language

 

Kapangidwe ka Mtsogoleri Wa Umulungu

Bucknell & KaundeChristian Leadership Seminar: The Making of a Godly Leader

7 Sessions English & Chichewa

 

 

Kuyenda ndi Yesu

Kukhala mwa Khristu

Kuyenda ndi YesuPamene Mulungu adapanikiza chidwi changa pondibvumbulitsira choonadi mmau ake, mwanjira ili yonse ndinayenere kulapa. Gawo la mau liri lonse lidakhala londitsegula maso anga a uzimu pa bvuto langa la uzimu. Ndidakhala Mkhristu kwa zaka zambiri, koma ziphunzitsozi zinafikira pa mfundo yoti zinandionetsa kukhala wosunthidwa kwambiri kupyolera nkuwerenga Baibulo. Koma ndithudi zinali zoposera ku werenga Baibulo. Ine ndidakumana ndi Mulungu, kapena ndinene Mulungu adali atakumana nane mkati mwenimweni mwa zosowa za mtima wanga zomwe sindinali kuzidziwa.

Makumanidwewo anali enieni zinali monga mzimu ananditengadi ndi kukandifikitsa pamalo pomwe ophunzira amapenyerera Yesu kapena kumafunsa iye mafunso. Mzimu anandipangitsa kuti ndione zomwe Yesu amazifikira. Iye kawirikawiri ndiponso mwamphabvu anali kundilankhula mu nthawi zimenezi, kotero zandipanga ine wokhulupirira wolimba ndi kufunikira kokhala Mkristu wonkhwima wokula msiknhu tsiku liri lonse mmoyo wake. Monga Paulo Mtumwi, ife sitinafikirebe pakukhala a ngwiro. Tiri ndi mwayi waukulu kwambiri kuti tikule msinkhu kuposera momwe timaganizira.

 

 


Top of page | Email us |BFF Homepage | Family Index


Biblical Foundations for Freedom